Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 16:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya;

2. kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zili zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.

3. Mulankhule Priska ndi Akula, anchito anzanga m'Kristu Yesu,

4. amene anapereka khosi lao cifukwa ca moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu;

5. ndipo mulankhule Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Mulankhule Epeneto wokondedwa wanga, ndiye cipatso coundukula ca Asiya ca kwa Kristu,

Werengani mutu wathunthu Aroma 16