Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 14:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe cinthu conyansa pa cokha; koma kwa ameneyo aciyesa conyansa, kwa iye cikhala conyansa.

15. Koma ngati iwe wacititsa mbale wako cisoni ndi cakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi cikondano. Usamuononga ndi cakudya cako, iye amene Kristu adamfera.

16. Cifukwa cace musalole cabwino canu acisinjirire,

17. Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala cakudya ndi cakumwa, koma cilungamo, ndi mtendere, ndi cimwemwe mwa Mzimu Woyera.

18. Pakuti iye amene atumikira Kristu mu izi akondweretsa Mulungu, nabvomerezeka ndi anthu.

19. Cifukwa cace tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzace.

20. Usapasule nchito ya Mulungu cifukwa ca cakudya. Zinthu zonse ziri zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.

21. Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusacita cinthu ciri conse cakukhumudwitsa mbale wako.

22. Cikhulupiriro cimene uli naco, ukhale naco kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu. Wodala ndiye amene sadziweruza mwini yekha m'zinthu zomwe iye wazibvomereza.

23. Koma iye amene akayika-kayika pakudya, atsutsika, cifukwa akudya wopanda cikhulupiriro; ndipo cinthu ciri conse cosaturuka m'cikhulupiriro, ndico ucimo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 14