Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 14:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma iwe uweruziranji mbale wako? kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? pakuti ife tonse tidzaimirira ku mpando wakuweruza wa Mulungu.

11. Pakuti kwalembedwa,Pali moyo wanga, ari Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine,Ndipo malilime onse adzabvomereza Mulungu,

12. Cotero munthu ali yense wa ife adzadziwerengera mlandu wace kwa Mulungu.

13. Cifukwa cace risaweruzanenso wina mnzace; koma weruzani ici makamaka, kuti munthu asaike cokhumudwitsa pa njira ya mbale wace, kapena compunthwitsa.

14. Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe cinthu conyansa pa cokha; koma kwa ameneyo aciyesa conyansa, kwa iye cikhala conyansa.

15. Koma ngati iwe wacititsa mbale wako cisoni ndi cakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi cikondano. Usamuononga ndi cakudya cako, iye amene Kristu adamfera.

16. Cifukwa cace musalole cabwino canu acisinjirire,

17. Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala cakudya ndi cakumwa, koma cilungamo, ndi mtendere, ndi cimwemwe mwa Mzimu Woyera.

18. Pakuti iye amene atumikira Kristu mu izi akondweretsa Mulungu, nabvomerezeka ndi anthu.

19. Cifukwa cace tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzace.

20. Usapasule nchito ya Mulungu cifukwa ca cakudya. Zinthu zonse ziri zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.

21. Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusacita cinthu ciri conse cakukhumudwitsa mbale wako.

Werengani mutu wathunthu Aroma 14