Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 13:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cikondano sicicitira mnzace coipa; cotero cikondanoco ciri cokwanitsa lao mulo.

11. Ndipo citani ici, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano cipulumutso cathu ciri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira.

12. Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; cifukwa cace tibvule nchito za mdima, ntibvale camuna ca kuunika.

13. Tiyendeyeode koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'cigololo ndi conyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.

14. Koma bvalani inu Ambuye Yesu-Kristu, ndipo musaganizire za thupi kucita zofuna zace.

Werengani mutu wathunthu Aroma 13