Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 11:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ngati zoundukula ziri zopatulika, coteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, coteronso nthambi.

17. Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wa kuthengo, unamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ace a mtengowo,

18. usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.

19. Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikamezetsanidwe nao.

20. Cabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi cikhulupiriro cako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:

21. pakuti ngati Mulungu sanaleka nthambi za mtundu wace, inde sadzakuleka iwe.

22. Cifukwa cace onani cifatso ndi kuuma mtima kwace kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwace; koma kwa iwe cifatso cace ca Mulungu, ngati ukhala cikhalire m'eifatsomo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.

23. Ndipo iwonso, ngati sakhala cikhalire ndi cisakhulupiriro, adzawamezanitsanso.

Werengani mutu wathunthu Aroma 11