Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 11:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuvanianitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakucokera kwa: akufa?

16. Ndipo ngati zoundukula ziri zopatulika, coteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, coteronso nthambi.

17. Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wa kuthengo, unamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ace a mtengowo,

18. usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.

19. Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikamezetsanidwe nao.

20. Cabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi cikhulupiriro cako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:

21. pakuti ngati Mulungu sanaleka nthambi za mtundu wace, inde sadzakuleka iwe.

22. Cifukwa cace onani cifatso ndi kuuma mtima kwace kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwace; koma kwa iwe cifatso cace ca Mulungu, ngati ukhala cikhalire m'eifatsomo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.

23. Ndipo iwonso, ngati sakhala cikhalire ndi cisakhulupiriro, adzawamezanitsanso.

24. Pakuti ngati iwe unasadzidwa ku mtengo wazitona wa mtundu wa kuthengo, ndipo unamezetsanidwa ndi mtengo wazitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wace, adzamezetsanidwa ndi mtengo wao womwewo wazitona?

25. Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa cinsinsi ici, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israyeli, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;

26. ndipo cotero Israyeli yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti,Adzaturuka ku Ziyoni Mpulumutsi;Iye adzacotsa zamwano kwa Yakobo:

27. Ndipo ici ndi cipangano canga ndi iwo,Pamene ndidzacotsa macimo ao.

Werengani mutu wathunthu Aroma 11