Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 11:12-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ngati kulakwa kwao kwatengera dzikolapansi zolemera, ndipo kucepa kwao klltengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao?

13. Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndiri mtumwi wa anthu amitundu, millemekeza utumiki wanga;

14. kuti ngati nkutheka ndikacititse nsanje amenewo a mtundu wanga; ndi kupulumutsa ena a iwo.

15. Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuvanianitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakucokera kwa: akufa?

16. Ndipo ngati zoundukula ziri zopatulika, coteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, coteronso nthambi.

17. Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wa kuthengo, unamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ace a mtengowo,

18. usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.

19. Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikamezetsanidwe nao.

20. Cabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi cikhulupiriro cako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:

21. pakuti ngati Mulungu sanaleka nthambi za mtundu wace, inde sadzakuleka iwe.

22. Cifukwa cace onani cifatso ndi kuuma mtima kwace kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwace; koma kwa iwe cifatso cace ca Mulungu, ngati ukhala cikhalire m'eifatsomo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.

23. Ndipo iwonso, ngati sakhala cikhalire ndi cisakhulupiriro, adzawamezanitsanso.

24. Pakuti ngati iwe unasadzidwa ku mtengo wazitona wa mtundu wa kuthengo, ndipo unamezetsanidwa ndi mtengo wazitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wace, adzamezetsanidwa ndi mtengo wao womwewo wazitona?

Werengani mutu wathunthu Aroma 11