Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 1:26-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Cifukwa ca ici Mulungu anawapereka iwo 1 ku zilakolako za manyazi; pakuti angakhale akazi ao anasandutsa macitidwe ao a cibadwidwe akhale macitidwe osalingana ndi cibadwidwe:

27. ndipo cimodzimodzinso amuna anasiya macitidwe a cibadwidwe ca akazi, natenthetsana ndi colakalaka cao wina ndi mnzace, amuna okhaokha anacitirana camanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.

28. Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'cidziwitso cao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukacita zinthu zosayenera;

29. anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, cinyengo, udani;

30. akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, acipongwe, odzitama, amatukutuku, ovamba zoipa, osamvera akuru ao,

31. opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda cikondi ca cibadwidwe, opanda cifundo;

32. amene ngakhale adziwa kuweruza kwace kwa Mulungu, kuti iwo 2 amene acita zotere ayenera imfa, azicita iwo okha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzicita.

Werengani mutu wathunthu Aroma 1