Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 1:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, kapolowa Yesu Kristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,

2. umene iye analonjeza kale ndi mau a ananeri ace m'malembo oyera,

3. wakunena za Mwana wace, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,

4. amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa ciyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Kristu Ambuye wathu;

5. amene ife tinalandira naye cisomo ndi utumwi, kuti amvere cikhulupiriro anthu a mitundu yonse cifukwa ca dzina lace;

6. mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Kristu;

7. kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Cisomo cikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.

8. Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu cifukwa ca inu nonse, cifukwa kuti mbiri ya cikhulupiriro canu idamveka pa dziko lonse lapansi.

9. Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, m'Uthenga Wabwino wa Mwana wace, kuti kosalekeza ndikumbukila inu, ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga,

Werengani mutu wathunthu Aroma 1