Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 3:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,

8. Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:

9. musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,

10. ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;

11. pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.

12. Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

13. kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

14. koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.

15. Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.

Werengani mutu wathunthu Akolose 3