Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 3:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;

6. cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;

7. zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,

8. Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:

9. musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,

10. ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;

11. pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.

12. Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

13. kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

14. koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.

15. Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.

16. Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.

17. Ndipo ciri conse mukacicita m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.

18. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.

Werengani mutu wathunthu Akolose 3