Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 3:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, funani zakumwamba, kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.

2. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

3. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Kristu mwa Mulungu,

4. Pamene Kristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.

5. Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;

6. cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;

7. zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,

8. Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:

9. musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,

10. ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;

11. pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.

12. Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

13. kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

Werengani mutu wathunthu Akolose 3