Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 2:8-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati cuma, mwa kukonda nzeru kwace, ndi cinyengo copanda pace, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu;

9. pakuti mwa iye cikhalira cidzalo ca Umulungu m'thupi,

10. ndipo muli odzazidwa mwa iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;

11. amenenso munadulidwa mwa iye ndi mdulidwe wosacitika ndi manja, m'mabvulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Kristu;

12. popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzindi iye m'cikhulupiriro ca macitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa iye kwa akufa.

13. Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;

14. adatha kutifafanizira ca pa ifeco colembedwa m'zoikikazo, cimene cinali cotsutsana nafe; ndipo anacicotsera pakatipo, ndi kucikhomera ici pamtanda;

15. atabvula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.

16. Cifukwa cace munthu aliyense asakuweruzeni inu m'cakudya, kapena cakumwa, kapena m'kunena tsiku la phwando, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;

17. ndizo mthunzi wa zirinkudzazo; koma thupi ndi la Kristu.

18. Munthu ali yense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzicepetsa mwini wace, ndikugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula cabe ndi zolingalira za thupi lace, wosagwiritsa mutuwo,

19. kucokera kwa iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempa, likula ndi makulidwe a Mulungu.

20. Ngati munafa pamodzi ndi Kristu kusiyana nazo zoyambaza dziko lapansi, mugonieranii ku zoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi,

21. usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza,

22. (ndizo zonse zakuonongedwa pocita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?

23. zimene ziri naotu manenedwe a nzeru m'kutumikira kwa cifuniro ca mwini wace, ndi kudzicepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma ziribe mphamvu konse yakuletsa cikhutitso ca thupi.

Werengani mutu wathunthu Akolose 2