Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 2:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. ndipo muli odzazidwa mwa iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;

11. amenenso munadulidwa mwa iye ndi mdulidwe wosacitika ndi manja, m'mabvulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Kristu;

12. popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzindi iye m'cikhulupiriro ca macitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa iye kwa akufa.

13. Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;

14. adatha kutifafanizira ca pa ifeco colembedwa m'zoikikazo, cimene cinali cotsutsana nafe; ndipo anacicotsera pakatipo, ndi kucikhomera ici pamtanda;

15. atabvula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.

16. Cifukwa cace munthu aliyense asakuweruzeni inu m'cakudya, kapena cakumwa, kapena m'kunena tsiku la phwando, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;

17. ndizo mthunzi wa zirinkudzazo; koma thupi ndi la Kristu.

18. Munthu ali yense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzicepetsa mwini wace, ndikugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula cabe ndi zolingalira za thupi lace, wosagwiritsa mutuwo,

Werengani mutu wathunthu Akolose 2