23. Pomwepo padafunika kuti 3 zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zeni zeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.
24. Pakuti 4 Kristu sanalowa m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m'Mwamba momwe, 5 kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu cifukwa ca ife;
25. kosati kuti adzipereke yekha kawiri kawiri; 6 monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika caka ndi caka ndi mwazi wosati wace;
26. cikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawiri kawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; kama tsopano 7 kamodzi pa citsirizo ca nthawizo waonekera kucotsa ucimo mwa nsembe ya iye yekha.
27. Ndipo popeza 8 kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo 9 atafa, ciweruziro;
28. kotero 10 Kristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza macimo a ambiri, 11 adzaonekera pa nthawi yaciwiri, wopanda ucimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira cipulumutso.