Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 9:2-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakuti cihema cidakonzeka, coyamba cija, m'menemo munali coikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika,

3. Koma m'kati mwa cophimba caciwiri, cihema conenedwa Malo Opatulikitsa;

4. okhala nayo mbale ya zofukiza yagolidi ndi likasa la cipangano, lokuta ponsepo ndi golidi, momwemo munali mbiya yagolidi yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idapukayo, ndi magome a cipangano;

5. ndi pamwamba pace akerubi a ulemerero akucititsa mthunzi pacotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano padera padera.

6. Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'cihema coyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;

7. koma kulowa m'caciwiri, mkuru wa ansembe yekha kamodzi pacaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka cifukwa ca iye yekha, ndi zolakwa za anthu;

8. Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo ku malo opatulika siinaonetsedwe, pokhala cihema coyamba ciri ciriri;

9. ndico ciphiphiritso ca ku nthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za cikumbu mtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.

10. Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyana-siyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.

11. Koma atafika Kristu, Mkuluwansembe wa zokoma zirinkudza, mwa cihema cacikuru ndi cangwiro coposa, cosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, cosati ca ciiengedweici,

12. kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi ana a ng'ombe, koma mwa mwazi wa iye yekha, analowa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo ciombolo cosatha.

13. Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira ciyeretso ca thupi;

14. koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

15. Ndipo mwa ici ali Nkhoswe ya cipangano catsopano, kotero kuti, popeza kudacitika imfa yakuombola zolakwa za pa cipangano coyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 9