Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 9:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pakuti pamene pali copangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo.

17. Pakuti copangiratu ciona mphamvu atafa mwini wace; popeza ciribe mphamvu konse pokhala wolemberayo ali ndi moyo;

18. momwemo coyambaconso sicinakonzeka copanda mwazi.

19. Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu once lamulo liri lonse monga mwa cilamulo, anatenga mwazi wa ana a ng'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,

20. nati, 1 Uwu ndi mwazi wa cipangano Mulungu adakulamulirani.

21. Ndiponso cihema ndi zotengera zonse za utumikiro anaziwaza momwemo ndi mwaziwo.

22. Ndipo monga mwa cilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo 2 wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.

23. Pomwepo padafunika kuti 3 zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zeni zeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 9