Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 9:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo cingakhale cipangano coyambaci cinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a pa dziko lapansi.

2. Pakuti cihema cidakonzeka, coyamba cija, m'menemo munali coikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika,

3. Koma m'kati mwa cophimba caciwiri, cihema conenedwa Malo Opatulikitsa;

4. okhala nayo mbale ya zofukiza yagolidi ndi likasa la cipangano, lokuta ponsepo ndi golidi, momwemo munali mbiya yagolidi yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idapukayo, ndi magome a cipangano;

5. ndi pamwamba pace akerubi a ulemerero akucititsa mthunzi pacotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano padera padera.

6. Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'cihema coyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;

7. koma kulowa m'caciwiri, mkuru wa ansembe yekha kamodzi pacaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka cifukwa ca iye yekha, ndi zolakwa za anthu;

Werengani mutu wathunthu Ahebri 9