2. Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa cihema coona, cimene Ambuye anacimanga, si munthu ai.
3. Pakuti mkulu wa ansembe ali yense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka,
4. Ndipo iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo;
5. amene atumikira cifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose acenjezedwa m'mene anafuna kupanga cihema: pakuti, Cenjera, ati, ucite zonse monga mwa citsanzoco caonetsedwa kwa iwe m'phiri.
6. Koma tsopano iye walandira citumikiro comveka coposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.