Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 7:15-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melikizedeke,

16. amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;

17. pakuti amcitira umboni,Iwe ndiwe wansembe nthawi yosathaMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.

18. Pakutitu kuli kutaya kwace kwa lamulo lidadza kalelo, cifukwa ca kufoka kwace, ndi kusapindulitsa kwace,

19. (pakuti cilamulo sicinacitira kanthu kakhale kopanda cirema), ndipo kulinso kulowa naco ciyembekezo coposa, cimene tiyandikira naco kwa Mulungu.

20. Ndipo monga momwe sikudacitika kopanda lumbiro;

21. (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro; koma iye ndi lumbiro mwa iye emeoe ananena kwa iye,Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa,Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).

22. Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.

23. Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe;

24. koma iye cifukwa kuti akhala iye nthawi yosatha ali nao unsembe wosasinthika,

25. kucokera komwekoakhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye, popeza ali nao moyo wace cikhalire wa kuwapembedzera iwo.

26. Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda coipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ocimwa, wakukhala wopitirira miyamba;

27. amene alibe cifukwa ca kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira cifukwa ca zoipa za iwo eni, yinayi cifukwa ca zoipa za anthu; pakuti ici anacita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.

28. Pakuti cilamulo cimaika akuru a ansembe anthu, okhala naco cifoko; koma mau a lumbirolo, amene anafika citapita cilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda cirema ku nthawi zonse.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 7