Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 5:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Monga anenanso mwina,Iwe ndiwe wansembe wa nthawizonseMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.

7. Ameneyo, m'masiku a thupi lace anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukuru ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,

8. angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo;

9. ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera iye cifukwa ca cipulumutso cosatha;

10. wochedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melikizedeke.

11. Za iye tirinao mau ambiri kuwanena, ndiotilaka powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu.

12. Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi cifukwa ca nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za ciyambidwe ca maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati cakudya cotafuna.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 5