Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 4:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Pakuti wanena pena za tsiku lacisanu ndi ciwiri, natero, Ndipo Mulungu anapumula tsiku lacisanu ndi ciwiri, kuleka nchito zace zonse

5. Ndipo m'menemonso,Ngati adzalowa mpumulo wanga.

6. Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowamo cifukwa ca kusamvera,

7. alangizanso tsiku lina, ndi kunena m'Davide, itapita nthawi yaikuru yakuti, Lero, monga kwanenedwakale,Lero ngati mudzamva mau ace,Musaumitse mitima yanu.

8. Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhuia m'tsogolomo za tsiku lina.

9. Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.

10. Pakuti iye amene adalowa mpumulo wace, adapumulanso mwini wace ku nchito zace, monganso Mulungu ku zace za iye.

11. Cifukwa cace ticite cangu ca kulowa mpumulowo, kuti f winaangagwe m'citsanzo comwe ca kusamvera.

12. Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ocitacita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

13. Ndipo palibe colengedwa cosaonekera pamaso pace, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pace pa iye amene ticita naye.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 4