Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 4:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Cifukwa cace ticite cangu ca kulowa mpumulowo, kuti f winaangagwe m'citsanzo comwe ca kusamvera.

12. Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ocitacita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

13. Ndipo palibe colengedwa cosaonekera pamaso pace, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pace pa iye amene ticita naye.

14. Popeza tsono tiri naye Mkuluwansembe wamkuru, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse cibvomerezo cathu.

15. Pakuti sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva cifundo ndi zofoka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda ucimo.

16. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 4