10. Pakuti iye amene adalowa mpumulo wace, adapumulanso mwini wace ku nchito zace, monganso Mulungu ku zace za iye.
11. Cifukwa cace ticite cangu ca kulowa mpumulowo, kuti f winaangagwe m'citsanzo comwe ca kusamvera.
12. Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ocitacita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
13. Ndipo palibe colengedwa cosaonekera pamaso pace, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pace pa iye amene ticita naye.