Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 2:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma timpenya iye amene adamcepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, cifukwa ca zowawa za imfa, wobvala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi cisomo ca Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu ali yense.

10. Pakuti kunamuyenera iye amene zonse ziri cifukwa ca iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa cipulumutso cao mwa zowawa.

11. Pakuti iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa acokera onse mwa mmodzi; cifukwa ca ici alibe manyazi kuwacha iwo abale,

12. ndi kuti,ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga,Pakati pa Mpingo ndidzakuyimbirani.

13. Ndiponso,Ndidzamtama Iye.Ndiponso,Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa,

14. Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;

15. nakamasule iwo onse amene, cifukwa ca kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

16. Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu.

17. Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wadfundo ndi wokhulupirika m'zinthu zakwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

18. Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 2