Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Yesu Kristu Nkhoswe yathu yakuposa angelo akhoza kumva nate cifundo

1. Mwa ici tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.

2. Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo colakwira ciri conse ndi cosamvera calandira mphotho yobwezera yolungama,

3. tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala cipulumutso cacikuru cotero? cimene Ambuye adayamba kucilankhula, ndipo iwo adacimva anatilimbikitsira ife;

4. pocita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikilo, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundu mitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa cifuniro cace.

5. Pakuti sanagoniersera angelo dziko lirinkudza limene tinenali.

6. Koma wina anacita umboni pena, nati,Munthu nciani kuti mumkumbukila iye?Kapena mwana wa munthu kuti muceza naye?

7. Munamcepsa pang'ono ndi angelo,Mudambveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu,Ndipo mudamuika iye wovang'anira nchito za manja anu;

8. Mudagonjetsa zonse pansi pa mapaziace.Pakuti muja adagonietsa zonse kwa iye, sanasiyapo kanthu kosamgoniera iye. Koma sitinayamba tsopano apa kuona zonse zimgonjera.

9. Koma timpenya iye amene adamcepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, cifukwa ca zowawa za imfa, wobvala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi cisomo ca Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu ali yense.

10. Pakuti kunamuyenera iye amene zonse ziri cifukwa ca iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa cipulumutso cao mwa zowawa.

11. Pakuti iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa acokera onse mwa mmodzi; cifukwa ca ici alibe manyazi kuwacha iwo abale,

12. ndi kuti,ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga,Pakati pa Mpingo ndidzakuyimbirani.

13. Ndiponso,Ndidzamtama Iye.Ndiponso,Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa,

14. Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;

15. nakamasule iwo onse amene, cifukwa ca kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

16. Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu.

17. Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wadfundo ndi wokhulupirika m'zinthu zakwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

18. Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.