Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 12:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsya moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,

19. ndi mau a lipenga, ndi maaenedwe a mau, manenedweamene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau;

20. pakuti sanakhoza kulola colamulidwaco. Ingakhale nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala;

21. ndipo maonekedwewo anali oopsa otere, kuti Mose anati, Ndiopatu ndi kunthunthumira.

22. Komatu mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wocuruka wa angelo,

23. ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,

24. ndi kwa Yesu Nkhoswe ya cipangano catsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula cokoma coposa mwazi wa Abeli.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 12