Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 11:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndi cikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anacitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;

6. koma wopanda cikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.

7. Ndi cikhulupiriro Nowa, pocenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pocita mantha, anamanga cingalawa ca kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yace; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa cilungamo ciri monga mwa cikhulupiriro.

8. Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kuturuka kunka ku malo amene adzalandira ngati colowa; ndipo anaturuka wosadziwa kumene akamukako.

9. Ndi cikhulupiriro anakhala mlendo ku dziko la lonjezano, losati lace, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isake ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;

10. pakuti analindirira mudzi wokhala nao maziko, mmisiri wace ndi womanga wace ndiye Mulungu.

11. Ndi cikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yace, popeza anamwerengera wokhulupirika iye amene adalonjeza;

12. mwa icinso kudacokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m'mwamba, ndi ngati mcenga, uli m'mbali mwa nyanja, osawerengeka.

13. Iwo onse adamwalira m'cikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.

14. Pakuti wo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.

15. Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.

16. Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 11