Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 11:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma cikhulupiriro ndico cikhazikitso ca zinthu zoyembekezeka, ciyesero ca zinthu zosapenyeka.

2. Pakuti momwemo akulu anacitidwa umboru.

3. Ndi cikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zocokera mwa zoonekazo.

4. Ndi cikhulupiriro Abeli anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kami, mene anacitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nacitapo umboni Mulungu pa mitulo yace; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.

5. Ndi cikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anacitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;

6. koma wopanda cikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 11