Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 5:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; cifukwa cace cirimikani, musakodwenso ndi gori la ukapolo.

2. Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Kristu simudzapindula naye kanthu.

3. Ndicitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kucita cilamulo conse.

4. Mulibe kanthu ndi Kristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana naco cisomo.

5. Pakuti ife mwa Mzimu, kucokera m'cikhulupiriro, tilindira ciyembekezo ca cilungamo,

6. Pakuti mwa Kristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu cikhulupiriro cakucititsa mwa cikondi.

7. Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere coonadi?

8. Kukopa kumene sikucokera kwa iye anakuitanani.

9. Cotupitsa pang'ono citupitsa mtanda wonse.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 5