Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 4:4-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wace, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,

5. kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.

6. Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wace alowe m'mitima yathu, wopfuula Abba, Atate.

7. Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.

8. Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munacitira ukapolo iyo yosakhalamilungu m'cibadwidwe cao;

9. koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofoka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuicitira ukapolo?

10. Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka.

11. Ndiopera inu, kuti kapena odadzibvutitsa ndi inu cabe.

12. Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndiri mongainu. Simunandicitira coipa ine;

13. koma mudziwa kuti m'kufoka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba:

14. ndipo cija ca m'thupi langa cakukuyesani inu simunacipeputsa, kapena sicinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Kristu Yesu mwini.

15. Pamenepo thamo lanu liri kuti? Pakuti ndikucitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.

16. Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona?

17. Acita cangu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawacitire iwowa cangu.

18. Koma nkwabwino kucita cangu m'zabwino nthawi zonse, si pokha pokha pokhala nanu pamodzi ine.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 4