Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 4:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. ndipo cija ca m'thupi langa cakukuyesani inu simunacipeputsa, kapena sicinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Kristu Yesu mwini.

15. Pamenepo thamo lanu liri kuti? Pakuti ndikucitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.

16. Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona?

17. Acita cangu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawacitire iwowa cangu.

18. Koma nkwabwino kucita cangu m'zabwino nthawi zonse, si pokha pokha pokhala nanu pamodzi ine.

19. Tiana tanga, amene ndirikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Kristu aumbika mwa inu,

20. koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; cifukwa ndisinkhasinkha nanu.

21. Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva cilamulo?

22. Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana amuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 4