Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 3:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma nkhoswe siiri ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.

21. Pamenepo kodi cilamulo citsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti cikadapatsidwa cilamulo eakukhoza kucitira moyo, cilungamo cikadacokera ndithu kulamulo.

22. Komatu lembo Iinatsekereza zonse pansi pa ucimo, kuti lonjezano la kwa cikhulupiriro ca Yesu Kristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.

23. Koma cisanadze cikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira cikhulupiriro cimene cikabvumbulutsidwa bwino bwino.

24. 1 Momwemo cilamulo cidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, 2 kuti tikayesedwe olungama ndi cikhulupiriro.

25. Koma popeza cadza cikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.

26. 3 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa cikhulupiriro ca mwa Yesu Kristu.

27. 4 Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.

28. 5 Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; 6 pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 3