Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 2:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma sitidawafumukira mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti coonadi ca Uthenga Wabwino cikhalebe ndi inu.

6. Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezera ine kanthu;

7. koma pena, pakuona kuti anaikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa, monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe

8. (pakuti iye wakucita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anacitanso mwa ine kundituma kwa amitundu);

9. ndipo pakuzindikira cisomoco cinapatsidwakwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Bamaba dzanja lamanja la ciyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;

10. pokhapo kuti tikumbukile aumphawi; ndico comwe ndinafulumira kucicita.

11. Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeyandinatsutsana naye pamaso pace, pakuti anatsutsika wolakwa.

12. Pakuti asanafike ena ocokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.

13. Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Bamabanso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.

14. Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa coonadi ca Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukangamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 2