Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 2:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mhelene, sanamkakamiza adulidwe;

4. ndico cifukwa ca abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tiri nao mwa Kristu Yesu, kuti akaticititse iukapolo.

5. Koma sitidawafumukira mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti coonadi ca Uthenga Wabwino cikhalebe ndi inu.

6. Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezera ine kanthu;

7. koma pena, pakuona kuti anaikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa, monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe

8. (pakuti iye wakucita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anacitanso mwa ine kundituma kwa amitundu);

9. ndipo pakuzindikira cisomoco cinapatsidwakwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Bamaba dzanja lamanja la ciyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;

10. pokhapo kuti tikumbukile aumphawi; ndico comwe ndinafulumira kucicita.

11. Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeyandinatsutsana naye pamaso pace, pakuti anatsutsika wolakwa.

12. Pakuti asanafike ena ocokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 2