1. Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Bamaba, ndinamtenganso Tito andiperekeze.
2. Koma ndinakwera kunkako mobvumbulutsa; ndipo ndinawauza Uthenga Wabwino umene ndiulalikira kwa amitundu; koma m'tseri kwa iwo omveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga cabe.
3. Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mhelene, sanamkakamiza adulidwe;
4. ndico cifukwa ca abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tiri nao mwa Kristu Yesu, kuti akaticititse iukapolo.
5. Koma sitidawafumukira mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti coonadi ca Uthenga Wabwino cikhalebe ndi inu.