Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 3:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikacigwire ici cimene anandigwirira Yesu Kristu.

13. Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,

14. ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.

15. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ici mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzabvumbulutsira inu;

16. cokhaci, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.

17. Abale khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife citsanzo canu.

18. Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawiri kawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Kristu;

19. citsiriziro cao ndico kuonongeka, mulungu wao ndiyo niimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amenealingirira za padziko.

20. Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; z kucokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Kristu;

21. amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lace la ulemerero, monga mwa macitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

Werengani mutu wathunthu Afilipi 3