Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 2:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,

6. ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,

7. koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;

8. ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

9. Mwa icinso Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,

10. kuti m'dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,

11. ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.

Werengani mutu wathunthu Afilipi 2