Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 2:26-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. popeza anali wolakalaka inu nonse, nabvutika mtima cifukwa mudamva kuti anadwala.

27. Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamcitira cifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale naco cisoni cionjezere-onjezere.

28. Cifukwa cace ndamtuma iye cifulumizire, kuti pakumuona mukakondwerenso, ndi inenso cindicepere cisoni.

29. Cifukwa cace mumlandire mwa Ambuye, ndi cimwemweconse; nimucitire ulemu oterewa;

30. pakuti cifukwa lea nchito ya Kristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wace, kuti z akakwaniritse ciperewero ca utumiki wanu wa kwa ine.

Werengani mutu wathunthu Afilipi 2