Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 2:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. kwaniritsani cimwemwe canga, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala naco cikondi comwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;

3. musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini;

4. munthu yense asapenyerere zace za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzaceo

5. Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,

6. ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,

7. koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;

8. ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

9. Mwa icinso Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,

10. kuti m'dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,

11. ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.

12. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani nchito yace ya cipulumutso canu ndi mantha, ndi kunthunthumira;

13. pakuti wakucita mwa inu kufuna ndi kucita komwe, cifukwa ca kukoma mtima kwace, ndiye Mulungu,

14. Citani zonse kopanda madandaulo ndi makani,

Werengani mutu wathunthu Afilipi 2