Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 2:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda cirema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,

16. akuonetsera mau a movo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira: nao m'tsiku la Kristu, kuti sindinathamanga cabe, kapena kugwiritsa nchito cabe.

17. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa cikhulupiriro canu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;

18. momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

19. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.

20. Pakuti ndiribe wina wa mtima womwewo, amene adza: samalira za kwa inu ndi mtima woona.

21. Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Kristu.

22. Koma muzindikira matsimikizidwe ace, kuti, monga mwana acitira atate wace, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.

23. Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posacedwa m'mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani;

24. koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga.

25. Koma ndinayesa nkufunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wanchito mnzanga ndi msilikari mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa cosowa canga;

26. popeza anali wolakalaka inu nonse, nabvutika mtima cifukwa mudamva kuti anadwala.

27. Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamcitira cifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale naco cisoni cionjezere-onjezere.

Werengani mutu wathunthu Afilipi 2