Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 2:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.

12. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani nchito yace ya cipulumutso canu ndi mantha, ndi kunthunthumira;

13. pakuti wakucita mwa inu kufuna ndi kucita komwe, cifukwa ca kukoma mtima kwace, ndiye Mulungu,

14. Citani zonse kopanda madandaulo ndi makani,

15. kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda cirema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,

16. akuonetsera mau a movo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira: nao m'tsiku la Kristu, kuti sindinathamanga cabe, kapena kugwiritsa nchito cabe.

17. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa cikhulupiriro canu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;

18. momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

19. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.

Werengani mutu wathunthu Afilipi 2