Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Afilipi 1:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Potero nciani? Cokhaco kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'coonadi, Kristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

19. Pakuti ndidziwa kuti ici cidzandicitira ine cipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Kristu;

20. monga mwa kulingiriritsa ndi ciyembekezo canga, kuti palibe cinthu cidzandicititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Kristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwamoyo, kapena mwa imfa.

21. Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Kristu, ndi kufa kuli kupindula.

22. Koma ngati kukhala ndi moyo m'thupi, ndiko cipatso ca nchito yanga, sindizindikiranso cimene ndidzasankha.

23. Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala naco colakalaka ca kucoka kukhala ndi Kristu, ndiko kwabwino koposa-posatu;

24. koma kukhalabe m'thupi ndiko kufunika koposa, cifukwa ca inu.

25. Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezeracimwemwe ca cikhulupiriro canu;

26. kuti kudzitamandira kwanu kucuruke m'Kristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.

27. Cokhaci, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Kristu: kuti, ndingakhale nditi ndirinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndiri kwina, ndikamva za kwa inu, kuti mucirimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi cikhulupiriro ca Uthenga Wabwino;

28. osaopa adani m'kanthu konse, cimene ciri kwa iwowa cisonyezo ca cionongeko, koma kwa inu ca cipulumutso, ndico ca kwa Mulungu;

29. kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu cifukwa ca Kristu, si kukhulupirira kwa iye kokha, komatunso kumva zowawa cifukwa ca iye,

30. ndi kukhala naco inu cilimbano comweci mudaciona mwa ine, nimukumva tsopano ciri mwa ine.

Werengani mutu wathunthu Afilipi 1