31. 1 Cifukwa ca ici munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wace; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.
32. Cinsinsi ici ncacikuru; koma ndinena ine za Kristu ndi Eklesia.
33. Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wace wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo 2 mkaziyo akumbukile kuti aziopa mwamuna.