Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 4:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'ciyembekezo cimodzi ca maitanidwe anu;

5. Ambuye mmodzi, cikhulupiriro cimodzi, ubatizo umodzi,

6. Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.

7. Ndipo kwa yense wa ife capatsika cisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu.

8. Cifukwa cace anena,M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,Naninkha zaufulu kwa anthu.

9. Koma ici, cakuti, Anakwera, nciani nanga komakuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?

10. Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.

11. Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi enaaneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;

12. kuti akonzere oyera mtima: ku nchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu;

13. kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa cikhulupiriro, ndi wa cizindikiritso ca Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa cidzaloca Kristu.

14. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengeka-tengeka ndi mphepo yonse ya ciphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kucenjerera kukatsata cinyengo ca kusoceretsa;

15. koma ndi kucita zoona mwa cikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira iye amene ali mutu ndiye Kristu;

16. kucokera mwa Iye thupi lonse, lokowanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kucititsa kwa ciwalo conse pa muyeso wace, licita makulidwe a thupi, kufikira cimango cace mwa cikondi.

17. Pamenepo ndinena ici, ndipo ndicita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'citsiru ca mtima wao,

Werengani mutu wathunthu Aefeso 4