Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 4:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa cikhulupiriro, ndi wa cizindikiritso ca Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa cidzaloca Kristu.

14. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengeka-tengeka ndi mphepo yonse ya ciphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kucenjerera kukatsata cinyengo ca kusoceretsa;

15. koma ndi kucita zoona mwa cikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira iye amene ali mutu ndiye Kristu;

16. kucokera mwa Iye thupi lonse, lokowanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kucititsa kwa ciwalo conse pa muyeso wace, licita makulidwe a thupi, kufikira cimango cace mwa cikondi.

17. Pamenepo ndinena ici, ndipo ndicita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'citsiru ca mtima wao,

18. odetsedwam'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, cifukwa ca cipulukiro ciri mwa iwo, cifukwa ca kuumitsa kwa mitima yao;

19. amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti acite cidetso conse mu umbombo.

20. Koma inusimunaphunzira Kristu cotero,

21. ngatitu mudamva iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa iye, monga coonadi ciri mwa Yesu;

22. kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za cinyengo;

Werengani mutu wathunthu Aefeso 4