14. Pakuti iye ndiye mtendere wathu, amene anacita kutionse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,
15. atacotsa udani m'thupi lace, ndiwo mau a cilamulo ca kuchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kucitapo mtendere;
16. ndi kuti akayanianitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;
17. ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;
18. kuti mwa iye ife tonse awiri tiri nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.
19. Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;
20. omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wa pangondya;
21. 1 mwa iye cimango conse, columikizika pamodzi bwino, cikula, cikhale 2 kacisi wopatulika mwa Ambuye;
22. 3 cimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale cokhalamo Mulungu mwa Mzimu.