Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 1:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a coonadi, Uthenga Wabwino wa cipulumutso canu; ndi kumkhulupirira iye, munasindikizidwa cizindikilo ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,

14. ndiye cikole ca colowa cathu, kuti ace ace akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wace uyamikike.

15. Mwa ici inenso, m'mene ndamva za cikhulupiriro'ca mwa Ambuye Yesu ciri mwa inu, cimenenso mufikitsira oyera mtima onse,

16. sindileka kuyamikacifukwa ca inu, ndi kukumbukila inu m'mapemphero anga;

17. kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire iye;

18. ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero wacolowa cace mwa oyera mtima,

19. ndi ciani ukuru woposa wa mphamvu yace ya kwa ife okhulupira, monga mwa macitidwe a mphamvu yace yolimba,

Werengani mutu wathunthu Aefeso 1