Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 1:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Kristu Yesu:

2. Cisomo kwa inu, ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.

3. Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu;

4. monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,

5. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana, a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace,

6. kuti uyamikidwe ulemerero wa cisomo cace, cimene anaticitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.

7. Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa, monga mwa kulemera kwa cisomo cace,

8. cimene anaticurukitsira ife m'nzeru zonse, ndi cisamaliro.

Werengani mutu wathunthu Aefeso 1