Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Timoteo 4:2-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. lalikira mau; cita nao pa nthawi yace, popanda nthawi yace; tsutsa, dzudzula, cenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi ciphunzitso.

3. Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:

4. ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe.

5. Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, cita nchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.

6. Pakuti ndirimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.

7. Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga cikhulupiriro:

8. cotsalira wandiikira ine korona wa cilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ace.

9. Tayesetsa kudza kwa ine msanga:

10. pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalimatiya.

11. Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira.

12. Koma Tukiko ndamtuma ku Efeso.

13. Copfunda cija ndinacisiya ku Trowa kwa Karpo, udze naco pakudza iwe, ndi mabuku, makamaka zikopa zija zolembedwa.

Werengani mutu wathunthu 2 Timoteo 4